Psalms 53

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide.

1Chitsiru chimati mu mtima mwake,
“Kulibe Mulungu.”
Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.

2Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano
pa ana a anthu
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
wofunafuna Mulungu.
3Aliyense wabwerera,
iwo onse pamodzi akhala oyipa;
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,
ngakhale mmodzi.

4Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;
anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,
ndipo sapemphera kwa Mulungu?
5Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu
pamene panalibe kanthu kochititsa mantha.
Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;
inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.

6Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!
Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,
lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!
Copyright information for NyaCCL